Genesis 42:32 - Buku Lopatulika tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri, koma mmodzi adamwalira, ndipo wamng'ono ali ndi bambo wathu ku Kanani.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri, abambo mmodzi. Mmodzi anamwalira, ndipo wamngʼono ali ndi abambo athu ku Kanaani.’ ” |
Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.
Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;
Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.