ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu;
Genesis 42:26 - Buku Lopatulika Ndipo anasenzetsa abulu ao tirigu wao nachokapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasenzetsa abulu ao tirigu wao nachokapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale akewo adasenzetsa abulu ao matumba a tirigu uja adagulayu, ndipo adanyamuka ulendo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abale a Yosefe aja anasenzetsa abulu awo tirigu amene anagula uja ndipo ananyamuka ulendo wawo. |
ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu;
koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho.
Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m'thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.
Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.