Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.
Genesis 42:23 - Buku Lopatulika Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe anali kumva zonse zimene ankakambiranazo, koma iwowo sadadziŵe, chifukwa choti ankalankhula naye kudzera mwa womasulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma sanadziwe kuti Yosefe ankawamva popeza kuti ankagwiritsa ntchito wotanthauzira poyankhula naye. |
Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.
Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa.
Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.
Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu.
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.