Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.
Genesis 42:14 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yosefe adaŵayankha kuti, “Paja ndanena kale kuti ndinu azondi basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yosefe anawawuza kuti, “Ndi momwe ndaneneramo: Inu ndinu akazitape. |
Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.
Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.