Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.
Genesis 41:56 - Buku Lopatulika Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono njalayo itakwanira dziko lonse, Yosefe adatsekula nkhokwe za tirigu zija, namaŵagulitsa Aejipitowo, chifukwa inali itakula ndithu mu Ejipitomo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene njala inafalikira dziko lonse, Yosefe anatsekula nkhokwe za zakudya namagulitsa tirigu kwa anthu a ku Igupto aja, pakuti njala inafika poyipa kwambiri mu Igupto monse. |
Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.
ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;
Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'mizinda, namsunge.
Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.
Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.
Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.
Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Tiro, ndipo iye adzabwerera kumphotho yake, nadzachita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.
Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira padziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili.
ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;