Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 41:50 - Buku Lopatulika

Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana aamuna awiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana amuna awiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zaka zanjala zisanafike, Yosefe adabereka ana aamuna aŵiri mwa Asenati uja, mwana wa Potifera, wansembe wa ku Oni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zisanafike zaka zanjala, Yosefe anabereka ana aamuna awiri mwa Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni.

Onani mutuwo



Genesis 41:50
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Ejipito.


Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.


Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.


Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.