Genesis 41:48 - Buku Lopatulika Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'mizinda; chakudya cha m'minda, yozinga mizinda yonse, anachisunga m'menemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'midzi; chakudya cha m'minda, yozinga midzi yonse, anachisunga m'menemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe adasonkhanitsa chakudya pa zaka zisanu ndi ziŵiri, pamene kunali dzinthu dzambirimbiri ku Ejipito, nadzisunga m'mizinda. Mu mzinda uliwonse ankasungamo chakudya cha ku minda yozungulira mzindawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yosefe anasonkhanitsa zakudya zonse zokololedwa mʼzaka zisanu ndi ziwiri zija ndipo anazisunga mʼmizinda. Mu mzinda uliwonse anayikamo chakudya chimene chinalimidwa mʼminda yozungulira komweko. |
Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.
Tsono anthu, anasunthira iwo kumizinda kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake.