Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Genesis 41:39 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Farao adauza Yosefe kuti, “Popeza kuti Mulungu wakuwonetsa zonsezi, palibenso wina aliyense wodziŵa zinthu ndi wanzeru kupambana iweyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anati kwa Yosefe, “Pakuti Mulungu wakudziwitsa iwe zonsezi, palibe wina wodziwa zinthu ndi wanzeru ngati iwe. |
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.
Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao.
Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Ejipito.
Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.
Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?
Pakuti chinthu achifuna mfumu nchapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuchiwulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu.
Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.