Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Genesis 41:37 - Buku Lopatulika Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao pamodzi ndi nduna zake adavomereza zonse zimene adaanena Yosefe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao ndi nduna zake anagwirizana nawo malangizo a Yosefe. |
Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake?
Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.
Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.
Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.
namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.
Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.