Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'mizinda, namsunge.
Genesis 41:36 - Buku Lopatulika Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha nthaŵi ya njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri imene idzabwere ndithu mu Ejipito muno, kuti choncho anthu a ku Ejipito asadzafe ndi njala.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chakudya chimenechi chisungidwe kuti chidzagwiritsidwe ntchito mʼzaka zisanu ndi ziwiri za njala imene ikubwerayo mu Igupto, kuti anthu a mʼdzikoli asadzafe ndi njalayo.” |
Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'mizinda, namsunge.