Farao achite chotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m'zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu.
Genesis 41:35 - Buku Lopatulika Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'mizinda, namsunge. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'midzi, namsunge. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zadzinthu zimene zikubwerazi. Azichita zonsezi ndi ulamuliro wanu, ndipo aziika tirigu padera m'mizinda yonse ndi kumsunga bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo asonkhanitse zakudya zonse za mʼzaka zabwino zikubwerazi. Pansi pa ulamuliro wa Farao, akuluakuluwo asonkhanitse ndi kusunga bwino tirigu mʼmizinda yonse. |
Farao achite chotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m'zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu.
Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.