Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
Genesis 41:28 - Buku Lopatulika Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono monga momwe ndanenera, ndiye kuti Mulungu wakuuziranitu zomwe adzachite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsono ndi monga ndafotokozeramu kuti Mulungu wakuwuziranitu zimene adzachite. |
Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.
Ndipo lotolo linabwerezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.
Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.