Genesis 41:18 - Buku Lopatulika ndipo taona, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo taona, zinatuluka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi yomweyo ndidangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zitatuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo ngʼombe zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zooneka bwino zinatuluka mu mtsinje muja ndi kumadya msipu wa mu mawango. |
ndipo taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinatuluka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Ejipito;
Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.
Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m'malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino.
Ndipo monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a mu Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Ejipito.