Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Genesis 41:17 - Buku Lopatulika Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa mtsinje; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Farao adati, “Ine ndidaalota ntaimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota nditayimirira mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, |
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
ndipo taona, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;