Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.
Genesis 41:13 - Buku Lopatulika Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo zidachitikadi monga momwe adaatimasulira. Ine ndidabwerera pa ntchito yanga, koma wophika buledi uja adampachika pa mtengo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo zinthu zinachitikadi monga mmene anatitanthauzira. Ine anandibwezera pa ntchito yanga ndipo winayo anapachikidwa.” |
Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.
Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale.
Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mzinda; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.