Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.
Genesis 41:10 - Buku Lopatulika Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja inu mfumu mudaatipsera mtima antchitofe. Ndipo ine ndi wophika buledi tonse mudaatitsekera m'ndende, m'nyumba ya mkulu wa alonda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paja nthawi ina Farao anapsera mtima antchito akefe, ndipo anatitsekera (ine ndi mkulu wa ophika buledi) mʼndende, mʼnyumba ya mkulu wa alonda. |
Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.
Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.