Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Genesis 40:23 - Buku Lopatulika Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe woperekera vinyo uja sadamkumbuke Yosefe, adangomuiŵaliratu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mkulu wa operekera zakumwa uja sanamukumbukire Yosefe ndipo anamuyiwaliratu. |
Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero.
Niti mfumu, Anamchitira Mordekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamchitire kanthu.
Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.