Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.
Genesis 40:22 - Buku Lopatulika Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma wophika buledi uja adampachika, monga momwe Yosefe adaanenera pomasulira maloto ao aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma mkulu wa ophika buledi anamupachika, mofanana ndi mmene Yosefe anatanthauzira maloto. |
Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.
akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.
Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova.
Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.
popeza mu Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.