akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.
Genesis 40:21 - Buku Lopatulika Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m'manja a Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m'manja a Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adamubwezera pa tchito yake woperekera vinyo uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Farao anamubwezera mkulu wa operekera zakumwa uja pa udindo wake, kotero kuti anayamba kuperekeranso zakumwa kwa Farao, |
akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.
Ndipo Farao anakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate.
Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika.
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.