Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.
Genesis 40:20 - Buku Lopatulika Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patangopitadi masiku atatu, padachitika phwando lokondwerera tsiku lobadwa Farao, ndipo Faraoyo adaitana nduna zake zonse. Tsono adamtulutsa uja woperekera vinyoyu pamodzi ndi wophika buledi yemwe uja. Aŵiri onse aja adaŵaimika pamaso pa nduna zake zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. |
Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.
akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.
akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.
Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;
chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake,
Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m'ndende;
Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.
Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya;