Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Genesis 40:15 - Buku Lopatulika chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inetu adachita chondiba, ndipo adabwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri. Tsono ngakhale kunoko, sindidachite kanthu kalikonse koti anditsekere nako m'ndende.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.” |
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.
Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamutu panga;
Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.
pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.
Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lake, aphedwe ndithu.
Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.
Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu.
achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.