Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.
Genesis 39:22 - Buku Lopatulika Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m'menemo, iye ndiye wozichita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m'menemo, iye ndiye wozichita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamsandutsa kapitao woyang'anira akaidi anzake onse, pamodzi ndi zonse zochitika m'ndendemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo. |
Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.
Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo.
mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.