ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja.
Genesis 39:19 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbuyake wa Yosefe adapsa mtima koopsa atamva mau a mkazi wake onena kuti, “Inde, izi ndi zimene wandichita kapolo wanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. |
ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja.
Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu.
Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.
Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;