anaitana aamuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau aakulu:
Genesis 39:17 - Buku Lopatulika Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono atabwera, adamsimbira nkhani yonseyo, adati, “Kapolo uja Wachihebri mudabwera naye m'nyumba munoyu, analoŵa kuchipinda kwanga kukandipunza ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. |
anaitana aamuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau aakulu:
ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja.
Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo?
Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.
chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;