ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo.
Genesis 39:16 - Buku Lopatulika Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwinjirowo adangousunga m'manja kudikira mpaka bwana wa Yosefe atabwera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. |
ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo.
Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine:
Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.