Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye.
Genesis 39:11 - Buku Lopatulika Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma tsiku lina Yosefe adaloŵa m'nyumba kuti agwire ntchito, ndipo panalibe antchito ena m'nyumbamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. |
Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye.
Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m'dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo.
Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira, ndi kuti, Palibe diso lidzandiona; navala chophimba pankhope pake.
Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;