Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.
Genesis 38:6 - Buku Lopatulika Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yuda adampezera mkazi mwana wake wachisamba uja Ere, dzina lake Tamara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yuda anamupezera mkazi mwana wake woyamba uja Eri, ndipo dzina la mkaziyo linali Tamara. |
Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.
Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.
ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;