Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Genesis 38:30 - Buku Lopatulika Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake mbale wake adabadwa chingwe chofiira chija chili lende ku dzanja. Tsono iyeyu adatchedwa Zera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake mʼbale wake amene anali ndi ulusi wofiira pa mkono wake uja anabadwa ndipo anapatsidwa dzina lakuti Zera. |
Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana aamuna onse a Yuda ndiwo asanu.
Ndi a ana a Zera: Yeuwele ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.
Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.
ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;