Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 38:29 - Buku Lopatulika

Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziphothyolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma mwanayo adalibweza dzanja lake, mwakuti mbale wake ndiye adayambira kubadwa. Tsono mzamba uja adati, “Uchita kudziphothyolera wekha chotere!” Motero mwanayo adatchedwa Perezi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma pamene anabweza mkonowo, mʼbale wake anabadwa ndipo mzamba anati, “Wachita kudziphotcholera wekha njira chonchi!” Ndipo anamutcha Perezi.

Onani mutuwo



Genesis 38:29
10 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga padzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa.


Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.


Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana aamuna onse a Yuda ndiwo asanu.


Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.


Ndipo mu Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;


Ana onse a Perezi okhala mu Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.


Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,


ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.