Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.
Genesis 38:26 - Buku Lopatulika Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yuda atazizindikira zinthuzo adati, “Akunenetsadi. Ndine amene ndidalakwa. Bwenzi nditampereka kwa mwana wanga Sela kuti amkwatire.” Choncho Yuda sadagone nayenso mkaziyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso. |
Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.
Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang'ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse.
Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi aang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.
Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.
Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zochimwa zako unazichita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'chilungamo chao, nawenso uchite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.
Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;
Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.
Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.
Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.