natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.
Genesis 38:25 - Buku Lopatulika Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akutengedwa kumene, Tamarayo adatumiza mau kwa Yuda mpongozi wake kuti, “Ine ndili ndi pathupi pa mwiniwake zinthu izi. Taziyang'anani, muwone mwina inu nkumudziŵa mwiniwakeyo kuti ndani: mpheteyi ndi chingwechi ndiponso ndodo yoyenderayi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?” |
natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.
Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.
Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.
Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;
tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.
Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.