Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.
Genesis 38:23 - Buku Lopatulika Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeze iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yuda adati, “Zinthu zimenezo atenge zikhale zake, kuwopa kuti anthu angadzatiseke. Ngakhale sudampeze mkaziyo, komabe ine ndidaamtumizira ndithu mbuziyi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.” |
Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.
Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.
Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.
Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa.
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.
(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)