Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.
Genesis 38:22 - Buku Lopatulika Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adabwerera kwa Yuda nakamuuza kuti, “Sindidampeze mkazi uja, ndipo anthu akumeneko andiwuza kuti, ‘Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ” |
Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.
Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeze iye.