Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole padzanja la mkazi; koma sanampeze iye.
Genesis 38:21 - Buku Lopatulika Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adafunsa anthu akomweko kuti, “Kodi mkazi wadama amene ankakhala pambali pa mseu wopita ku Enaimu uja ali kuti?” Anthuwo adayankha kuti, “Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?” Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.” |
Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole padzanja la mkazi; koma sanampeze iye.
Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.
Unamanga chiunda chako pa mphambano zilizonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kuchulukitsa chigololo chako.