Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.
Genesis 38:17 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yuda adayankha kuti, “Ndidzakutumizira mbuzi yaing'ono ya m'khola mwanga.” Tsono Tamarayo adati, “Chabwino, ndivomera mukandipatsa chikole choti mpaka mudzanditumizire.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.” Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?” |
Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.
Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.
Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole padzanja la mkazi; koma sanampeze iye.
Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini.
Anthu amaninkha akazi onse achigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kuchokera kumbali zonse, kuti achite nawe chigololo.
Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.
Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo.