Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.
Genesis 38:15 - Buku Lopatulika Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yuda atamuwona, adaamuyesa mkazi wadama, chifukwa anali atadziphimba kumaso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope. |
Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.
Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.
Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.