Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Genesis 37:7 - Buku Lopatulika pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tonsefe tinali m'munda, ndipo tinalikumanga mitolo yatirigu. Tilikumanga chomwecho, mtolo wanga unaimirira. Tsono mitolo yanu inauzungulira mtolo wangawo ndi kumauŵeramira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife timamanga mitolo ya tirigu ku munda ndipo mwadzidzidzi mtolo wanga unayimirira chilili, pamene mitolo yanu inazungulira mtolo wangawo nʼkumawugwadira.” |
Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.
Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.
Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.
Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.
Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake.
Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.
Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.
kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,
Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.