Genesis 37:6 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adaŵauza kuti “Mverani maloto omwe ndalota. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawawuza kuti, “Tamvani maloto amene ndinalota: |
pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.
Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.
Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.
Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu paphiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.