Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m'manja mwao, ambwezenso kwa atate wake.
Genesis 37:23 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe atafika kumene kunali abale akewo, iwowo adamuvula mkanjo wake, uja wautali wamanjawu umene adaavala, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yosefe atafika kwa abale ake, iwo anamuvula mkanjo wake wamanja aatali uja umene anavala |
Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m'manja mwao, ambwezenso kwa atate wake.
ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo.
Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.
Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.
Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye.