Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.
Genesis 37:18 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale ake aja adamuwonera kutali, iye asanayandikire nkomwe pamene panali iwopo. Adayamba kumpangira chiwembu natsimikiza zoti amuphe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abale ake aja anamuonera patali. Ndipo asanafike nʼkomwe kumene kunali iwo kuja, anayamba kale kumupangira chiwembu choti amuphe. |
Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.
Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.
Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.
Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.
Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.
Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;
Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.
Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:
Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;
Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.