Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.
Genesis 37:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anakhala m'dziko limene anakhalamo mlendo atate wake, m'dziko la Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anakhala m'dziko limene anakhalamo mlendo atate wake, m'dziko la Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe adakhalabe ku dziko la Kanani kumene bambo wake ankakhala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo ankakhala mʼdziko la Kanaani kumene abambo ake ankakhala. |
Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.
Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.
akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.
mfumu Magadiele, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m'dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu.
Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoze kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao.