Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 36:9 - Buku Lopatulika

Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi:

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi:

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu, okhala m'dziko lamapiri la Seiri.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.

Onani mutuwo



Genesis 36:9
10 Mawu Ofanana  

Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.


Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.


Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:


amenewa ndi maina a ana aamuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wake wa Esau, Reuwele mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wake wa Esau.


mfumu Magadiele, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m'dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu.


Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.


Ndipo ena a iwowa a ana a Simeoni, amuna mazana asanu, ananka kuphiri la Seiri; akuwatsogolera ndiwo Pelatiya, ndi Neariya, ndi Refaya, ndi Uziyele; ana a Isi.


Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.


musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake.


Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.