Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.
Genesis 36:5 - Buku Lopatulika ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana aamuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana amuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo Oholibama adabala Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndi ana amene adabereka Esau m'dziko la Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani. |
Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.
Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora.
Amenewa ndi ana aamuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau.
Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake.