Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti.
Genesis 36:4 - Buku Lopatulika Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reuwele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reuwele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ada adamubalira Esau Elifazi. Basemati adabala Reuele Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; |
Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti.
ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana aamuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani.
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.