Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
Genesis 36:2 - Buku Lopatulika Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Esau anatenga akazi ake a ana akazi a m'Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Esau adaakwatira akazi Achikanani aŵa: Ada mwana wa Eloni Muhiti, Oholibama mwana wa Ana, mwana wa Zibiyoni Muhivi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi |
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
ndipo Esau ananka kwa Ismaele, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismaele mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake.
Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora.
Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake.