Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
Genesis 36:12 - Buku Lopatulika Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wake wa Esau. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa (Timna anali mzikazi wa Elifazi mwana wa Esau, ndipo mwa Timnayo Elifazi adaberekamo Amaleke.) Ameneŵa ndiwo ana a Ada mkazi wa Esau. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau. |
Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
Ndi ana aamuna a Reuwele: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wake wa Esau.
Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.