kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;
Genesis 36:1 - Buku Lopatulika Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nazi zidzukulu za Esau, amene ankatchedwanso Edomu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu: |
kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;
Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.
Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anachita mobwezera chilango pa nyumba ya Yuda, napalamula kwakukulu pakuibwezera chilango,
Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.
Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga.