Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Genesis 34:9 - Buku Lopatulika Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu aakazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tiyeni tikhale ogwirizana chifukwa cha ukwati umenewu. Ife tidzakwatira ana anu, inunso mudzakwatira ana athu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tiyeni tichite mgwirizano wa ukwati kuti ife tidzikwatira ana anu ndi inu mudzikwatira ana athu. |
Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.
Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake.
kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatirana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?
Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.