Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.
Genesis 34:8 - Buku Lopatulika Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Hamori adaŵauza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamkonda mwana wanu. Chonde muloleni kuti amukwatire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Hamori anawawuza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamukonda kwambiri mwana wanu. Chonde muloleni kuti akhale mkazi wake. |
Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.
Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.
Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu aakazi.
a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.