Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake aamuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo.
Genesis 34:6 - Buku Lopatulika Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Hamori, bambo wa Sekemu, adapita kukacheza ndi Yakobe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Hamori, abambo a Sekemu, anapita kukakambirana ndi Yakobo. |
Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake aamuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo.
Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.
Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?